Total Pageviews

Monday, April 20, 2009

Ode to Kabula CityCan my love for Kabula, so different from my love for Zomba (paTexas) be aptly described? If so, let it be proved:

Kodi iwe Kabula
paja ati ndiwe Blantyre tsopano
Ah, iwe Kabula!
Ndimakumbuka ndili mwana
kundiwopsyeza ati
"Iwe ukapanda ku kwecha nkhali siwu pita nawo ku Blantyre."
Inetu nthawi yomweyo ku kwecha nkhali mpaka nkhali kubowoka

Ah, Kabula
kodi ndi zowona?
Kuti nthawi imeneyo anthu otchena onse ama shopa ma georgette kumeneko?
Panalinso ma shati aja onyezimila thwani thwani, ati Viscose
amapezeka kumeneko mu shopu ija ya ku Joni inathyoledwa ija?

Ine ndimakumbuka
kumvera pa Radio MBC, 'broadcasting from Blantyre'
nyimbo ya "zinabwera mochedwa inu a Phiri"
kodi ndi nyimbo imene ija anatchulamo
Delamere House kuti ndi nyumba yokwera pa mwamba pa inzake
zosowatu izo

Nanga ma red star
a city ovala za orange
6 July
ma fana a ku Dharap
atsikana a pa Our Lady
Amwenye a ku Mpingwe
ma Double Decker
ku Zoo ndi ku Museum

Iyayi ife kunali ku silira
moyo wa ntauni monga muja anayimbira Peter Pine monga mwa dzina lake nthawi imeneyo
Tinakhalako mochedwa
cha mu Chiwembe ndi mu Nkhumbemu
koma sizinali chimodzi modzi
double decker inali kunka kumapeto
timakwela ya Mbayani, ya Chileka ndi ya Lunzu popita ku Nkhumbe
ya Highway, popita ku Chiwembe
Kondodo nd PTC ati kuyiphatikiza limodzi pansi phiii
kaya nkutulukila achina Peoples
kenaka kanyama kaja ati Shoprite
kuchokela komwe ku Joni
ayi sizinali chimodzi modzi

Pano ati ndinu a Blantyre
u Kabula uja umakuyanjani
koma zija ndizakale
pana tiyende nawo mu Highway
popita ku Game
ana aku Poly nangatu a poyila
a panga bwanji chipolowe Highway m'mene ikuwopsyera
kayatu kaya
tizawona nawo turf,
kumeneko ku Blantyre.....

end of Part One.
pic: http://z.about.com/d/goafrica/1/0/5/8/blantyre.jpg

No comments: